8 Pakuti padzakhala tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, kuti ndidzatyola gori lace pakhosi pako, ndipo ndidzadula zomangira zako; ndipo alendo sadzamuyesanso iye mtumiki wao;
9 koma adzamtumikira Yehova Mulungu wao, ndi Davide mfumu yao, imene ndidzawaukitsira.
10 Ndipo usaope, iwe Yakobo mtumiki wanga, ati Yehova; usaope, iwe Israyeli; pakuti, taona, ndidzakupulumutsa iwe kutari, ndi mbeu zako ku dziko la undende wao; ndipo Yakobo adzabwera, nadzakhala ndi mtendere, ndipo adzakhala cete, palibe amene adzamuopsya.
11 Pakuti Ine ndiri ndi iwe, ati Yehova, kuti ndipulumutse iwe; koma ndidzatha ndithu amitundu onse amene ndinakumwazira mwa iwo, koma sindidzatha iwe ndithu; koma ndidzakulangiza iwe ndi ciweruziro, ndipo sindidzakuyesa wosaparamula.
12 Pakuti atero Yehova, Kulaswa kwako kuti kosapoleka ndi bala lako liri lowawa.
13 Palibe amene adzanenera mlandu wako, ulibe mankhwala akumanga nao bala lako.
14 Mabwenzi ako onse anakuiwala iwe; salikukufuna iwe; pakuti ndakulasa ndi bala la mdani, ndi kulanga kwa wankhanza; cifukwa ca mphulupulu yako yaikuru, cifukwa zocimwa zako zinacuruka.