1 Mau amene anadza kwa Yeremiya kucokera kwa Yehova caka cakhumi ca Zedekiya mfumu ya Yuda, cimene cinali caka cakhumi ndi cisanu ndi citatu ca Nebukadirezara.
2 Nthawi yomweyo nkhondo ya mfumu ya Babulo inamangira Yerusalemu misasa; ndipo Yeremiya mneneri anatsekeredwa m'bwalo la kaidi, linali ku nyumba ya mfumu ya Yuda.
3 Pakuti Zedekiya mfumu ya Yuda inamtsekera iye, nati, Cifukwa canji ulinkunenera, kuti, Yehova atero, Taonani, ndidzapereka mudzi uwu m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo iye adzaulanda,
4 ndipo Zedekiya mfumu ya Yuda sadzapulumuka m'dzanja la Akasidi, koma adzaperekedwadi m'dzanja la mfumu ya Babulo, ndipo adzanena ndi iye pakamwa ndi pakamwa, ndipo adzaonana maso ndi maso;
5 ndipo adzatsogolera Zedekiya kunka ku Babulo, ndipo adzakhala komwe kufikira ndidzamzonda, ati Yehova: ngakhale mudzamenyana ndi Akasidi, simudzapindula konse?
6 Ndipo Yeremiya anati, Mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,