19 wamkuru, m'upo, wamphamvu m'nchito; maso anu ali otsegukira njira zonse za ana a anthu; kuti mupatse yense monga mwa cipatso ca macitidwe ace;
20 amene munaika zizindikiro ndi zodabwitsa m'dziko la Aigupto, mpaka lero lomwe, m'Israyeli ndi mwa anthu ena; nimunadzitengera mbiri, monga lero lomwe;
21 ndipo munaturutsa anthu anu Israyeli m'dziko la Aigupto ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;
22 ndipo munawapatsa iwo dziko ili, limene munalumbirira makolo ao kuti mudzawapatsa, dziko moyenda mkaka ndi uci;
23 ndipo analowa, nakhalamo; koma sa namvera mau anu, sanayenda m'cilamulo canu; sanacita kanthu ka zonse zimene munawauza acite; cifukwa cace mwafikitsa pa iwo coipa conseci;
24 taonani mitumbira, yafika kumudzi kuugwira, ndipo mudzi uperekedwa m'dzanja la, Akasidi olimbana nao, cifukwa ca lupanga, ndi cifukwa ca njala, ndi cifukwa ca caola; ndipo cimene munacinena caoneka; ndipo, taonani, muciona.
25 Ndipo Inu Yehova Mulungu mwati kwa ine, Udzigulire munda ndi ndalama, nuitane mboni; koma mudzi waperekedwa m'manja a Akasidi.