36 Cifukwa cace tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babulo ndi lupanga, ndi njala, ndi caola:
37 Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapitikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukuru, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,
38 ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;
39 ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwacitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
40 ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawacokera kuleka kuwacitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandicokere.
41 Inde, ndidzasekerera iwo kuwacitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
42 Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa coipa conseci, comweco ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonieza.