38 ndipo adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao;
39 ndipo ndidzawapatsa mtima umodzi ndi njira imodzi, kuti andiope Ine masiku onse; kuwacitira zabwino, ndi ana ao pambuyo pao;
40 ndipo ndidzapangana nao pangano lamuyaya, kuti sindidzawacokera kuleka kuwacitira zabwino; koma ndidzalonga kuopsa kwanga m'mitima yao, kuti asandicokere.
41 Inde, ndidzasekerera iwo kuwacitira zabwino, ndipo ndidzawaoka ndithu m'dziko lino ndi mtima wanga wonse ndi moyo wanga wonse.
42 Pakuti atero Yehova: Monga ndatengera anthu awa coipa conseci, comweco ndidzatengera iwo zabwino zonse ndawalonieza.
43 Ndipo minda idzagulidwa m'dziko lino, limene muti, Ndilo bwinja, lopanda munthu kapena nyama; loperekedwa m'dzanja la Akasidi.
44 Anthu adzagula minda ndi ndalama, adzalembera akalata ogulira, adzawasindikiza, adzaitana mboni, m'dziko la Benjamini, ndi m'malo ozungulira Yerusalemu, ndi m'midzi ya Yuda, ndi m'midzi ya kumtunda, ndi m'midzi ya kucidikha, ndi m'midzi ya ku Mwera; pakuti ndidzabweza undende wao, ati Yehova.