9 ngakhale kudzimangira nyumba zokhalamo; ndipo sitiri nao munda wamphesa, kapena munda, kapena mbeu;
10 koma takhala m'mahema, ntimvera, nticita monga mwa zonse anatiuza Yonadabu kholo lathu.
11 Koma panali, pamene Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo anadza m'dzikomu, ife tinati, Tiyeni tinke ku Yerusalemu cifukwa tiopa nkhondo ya Akasidi, ndi nkhondo ya Aramu; ndipo tikhala m'Yerusalemu.
12 Ndipo anadza mau a Yehova kwa Yeremiya, kuti,
13 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli: Pita, nunene kwa anthu a Yuda ndi kwa okhala m'Yerusalemu, Kodi simudzalola kulangizidwa kumvera mau anga ati Yehova.
14 Mau a Yonadabu mwana wa Rekabu, amene anauza ana ace, asamwe vinyo, alikucitidwa, ndipo mpaka lero samamwa, pakuti amvera lamulo la kholo lao; koma Ine ndanena ndi inu, ndalawirira ndi kunena; koma simunandimvera Ine.
15 Ndatumanso kwa inu atumiki anga onse aneneri, ndalawirira ndi kuwatuma, kuti, Bwererani kuleka yense njira yace yoipa, konzani macitidwe anu, musatsate milungu yina kuitumikira, ndipo mudzakhala m'dziko limene ndakupatsani inu ndi makolo anu; koma simunandichera khutu lanu, simunandimvera Ine.