24 Ndipo Zedekiya anati kwa Yeremiya, Anthu asadziwe mau amene, ndipo sudzafa.
25 Koma akamva akuru kuti ndalankhula ndi iwe, nakafika kwa iwe, ndi kuti kwa iwe, Utifotokozere ife comwe wanena kwa mfumu; osatibisira ici, ndipo sitidzakupha iwe; ndiponso zomwe mfumu inanena kwa iwe;
26 pamenepo uziti kwa iwo, Ndinagwa ndi pembedzero langa pamaso pa mfumu, kuti asandibwezerenso ku nyumba ya Yonatani ndifere komweko.
27 Ndipo akuru onse anadza kwa Yeremiya, namfunsa; ndipo iye ananena nao monga mwa mau onsewo anamuuza mfumu. Ndipo analeka kunena naye; pakuti sikunamveka mlandu.
28 Ndipo Yeremiya anakhala m'bwalo la kaidi mpaka dzuwa lakugwidwa Yerusalemu. Ndipo anali komweko pogwidwa Yerusalemu.