1 Ngati udzabwera, Israyeli, ati Yehova, udzabwera kwa Ine; ndipo ngati udzacotsa zonyansa zako pamaso panga sudzacotsedwa.
2 Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'ciweruziro, ndi m'cilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
3 Pakuti Yehova atero kwa anthu a Yuda ndi kwa Yerusalemu, Limani masala anu, musabzale paminga.
4 Mudzidulire nokha kwa Yehova, cotsani khungu la mitima yanu, amuna inu a Yuda ndi okhala m'Yerusalemu; ukali wanga ungaturuke ngati moto, ungatenthe kuti sangathe kuuzima, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe anu.
5 Nenani m'Yuda, lalikirani m'Yerusalemu, ndi kuti, Ombani lipenga m'dzikomo; pfuulani, ndi kuti, Sonkhanani pamodzi, tilowe m'midzi ya malinga.
6 Kwezani mbendera kuyang'ana ku Ziyoni; thawani kuti mupulumuke, musakhale; pakuti ndidza ndi coipa cocokera kumpoto ndi kuononga kwakukuru.