10 Pakuti tsikulo ndi la Ambuye, Yehova wa makamu, tsiku lakubweza cilango, kuti abwezere cilango adani ace; ndipo lupanga lidzadya, lidzakhuta, nilidzamwetsa mwazi wao; pakuti Ambuye, Yehova wa makamu, ali ndi nsembe m'dziko la kumpoto pa nyanja ya Firate.
11 Kwera ku Gileadi, tenga bvunguti, namwali iwe mwana wa Aigupto; wacurukitsa mankhwala cabe; palibe kucira kwako.
12 Amitundu amva manyazi anu, dziko lapansi ladzala ndi kupfuula kwanu; pakuti amphamvu akhumudwitsana, agwa onse awiri pamodzi.
13 Mau amene Yehova ananena kwa Yeremiya mneneri, kuti Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo adzafika adzakantha dziko la Aigupto.
14 Nenani m'Aigupto, lalikirani m'Migidoli, lalikirani m'Nofi ndi Tapanesi; nimuti, Udziimike, nudzikonzere wekha; pakuti lupanga ladya pozungulira pako.
15 Akulimba ako akokoledwa bwanji? sanaime, cifukwa Yehova anawathamangitsa,
16 Anapunthwitsa ambiri, inde, anagwa wina pa mnzace, ndipo anati, Ukani, tinkenso kwa anthu athu, ku dziko la kubadwa kwathu, kucokera ku lupanga lobvutitsa.