5 Pakuti adzakwera pa cikweza ca Luhiti ndi kulira kosaleka; pakuti pa citsiko ca Horonaimu amva kulira kowawa kwa cionongeko.
6 Thawani, pulumutsani miyoyo yanu, mukhale amarisece m'cipululu,
7 Pakuti, cifukwa wakhulupirira nchito zanu ndi cuma canu, iwenso udzagwidwa; ndipo Kemosi adza kundende, ansembe ace ndi akuru ace pamodzi.
8 Ndipo wakufunkha adzafikira pa midzi yonse, sudzapulumuka mudzi uli wonse; cigwa comwe cidzasakazidwa, ndipo cidikha cidzaonongedwa; monga wanena Yehova.
9 Patsani Moabu mapiko, kuti athawe apulumuke; midzi yace ikhale bwinja, lopanda wokhalamo.
10 Atembereredwe iye amene agwira nchito ya Yehova monyenga, atembereredwe iye amene abweza lupanga lace kumwazi.
11 Moabu wakhala m'mtendere kuyambira ubwana wace, wakhala pansenga, osatetekulidwa, sananke kundende; cifukwa cace makoleredwe ace alimobe mwa iye, pfungo lace silinasinthika.