41 Taonani, anthu acokera kumpoto; ndiwo mtundu waukuru, ndipo mafumu ambiri adzaukitsidwa kucokera ku malekezero a dziko lapansi.
42 Agwira uta ndi nthungo; ali ankharwe, alibe cifundo; mau ao apokosera ngati nyanja, ndipo akwera akavalo, yense aguba monga munthu wa kunkhondo, kukamenyana ndi iwe, mwana wamkazi wa Babulo.
43 Mfumu ya ku Babulo yamva mbiri yao, ndipo manja ace alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.
44 Taonani, mtundu uja adzakwerera mudzi wolimba ngati mkango wocokera ku Yordano wosefuka; koma dzidzidzi ndidzauthamangitsa umcokere, ndipo ali yense amene asankhidwa, ndidzamuika woyang'anira wace; pakuti wakunga Ine ndani? adzandiikira nthawi ndani? ndipo mbusa adzaima pamaso panga ndani?
45 Cifukwa cace tamvani uphungu wa Yehova, umene waupangira pa Babulo; ndi zimene walingirira dziko la Akasidi; ndithu adzawakoka, ana ang'ono a zoweta; ndithu adzayesa busa lao bwinja pamodzi nao.
46 Dziko lapansi linthunthumira, pa phokoso la kugwidwa kwa Babulo, ndipo mpfuu wamveka mwa amitundu.