17 Kodi suona iwe cimene acicita m'midzi ya Yuda ndi m'miseu ya Yerusalemu?
18 Ana atola nkhuni, atate akoleza moto, akazi akanyanga ufa, kuti aumbe mikate ya mfumu yaikazi ya kumwamba, athirire milungu yina nsembe yothira, kuti autse mkwiyo wanga.
19 Kodi autsa mkwiyo wanga? ati Yehova; kodi sadziutsira okha manyazi a nkhope zao?
20 Cifukwa cace, ati Ambuye Mulungu, Taonani, mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzathiridwa pa malo ano, pa anthu, ndi pa nyama, ndi pa mitengo ya m'munda, ndi pa zipatso zapansi; ndipo udzatentha osazima.
21 Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli; Ikani zopereka zopsereza zanu pa nsembe zophera zanu, nimudye nyama.
22 Pakuti sindinanena kwa makolo anu, tsiku lija ndinawaturutsa m'dziko la Aigupto, ngakhale kuwauza nsembe zopsereza kapena zophera;
23 koma cinthu ici ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti cikukomereni.