23 koma cinthu ici ndinawauza, kuti, Mverani mau anga, ndipo ndidzakhala Mulungu wanu, ndipo inu mudzakhala anthu anga; nimuyende m'njira yonse imene ndakuuzani inu, kuti cikukomereni.
24 Koma sanamvera, sanachera khutu, koma anayenda m'upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera cambuyo osayenda m'tsogolo.
25 Ciyambire tsiku limene makolo anu anaturuka m'dziko la Aigupto kufikira lero lino, ndatumiza kwa inu atumiki anga onse, aneneri, tsiku ndi tsiku, kuuka mamawa ndi kuwatumiza iwo;
26 koma sanandimvera Ine, sanacherakhutu lao, koma anaumitsa khosi lao; anaipa koposa makolo ao.
27 Ndipo uzinena kwa iwo mau awa onse, koma sadzakumvera iwe; ndipo udzawaitananso; koma sadzakuyankha iwe.
28 Ndipo udzati kwa iwo, Umene ndi mtundu wosamvera mau a Yehova Mulungu wao, wosalola kulangizidwa, coonadi catha, cadulidwa pakamwa pao.
29 Senga tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti se; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.