1 Pamenepo anaturuka nane kumka ku bwalo la kunja, njira ya kumpoto; nalowa nane ku nyumba yazipinda idali pandunji pa mpatawo, ndi pandunji pa nyumbayo inaloza kumpoto.
2 Cakuno ca m'litali mwace mwa mikono zana limodzi kunali khomo la kumpoto, ndi kupingasa kwace mikono makumi asanu.
3 Pandunji pa mikono makumi awiri a bwalo lam'kati, ndi pandunji pa moyalamo mwa miyala, mwa bwalo lakunja, panali khonde lam'mwamba, lokomana ndi khonde linzace losanjikika paciwiri.
4 Ndi kukhomo kwa zipinda anakonza poyendapo, kupingasa kwace mikono khumi m'kati mwace, njira ya mikono zana limodzi, ndi makomo ao analoza kumpoto.
5 Ndipo zipinda zapamwamba zinacepa, pakuti makonde am'mwamba analanda pamenepo, cifukwa cace zinacepa koposa zapansi ndi zapakati m'nyumba yazipinda.
6 Pakuti zinasanjikizana pawiri, ndipo zinalibe nsanamira ngati nsanamira za kumabwalo; cifukwa cace zam'mwambazo zinacepa koposa zakunsi ndi zapakati kuyambira pansi.
7 Ndipo linga linali kunialo, loli'ngana ndi nyumba yazipinda, kuloza ku bwalo lakunja, popenyana ndi nyumba yazipinda, m'litali mwace munali mikono makumi asanu.