5 Nati kwa enawo, nditikumva ine, Pitani pakati pa mudzi kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekerere, musacite cifundo;
6 iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikira munthu ali yense ali naco cizindikilo, ndipo muyambe pa malo anga opatulika, Pamenepo anayamba ndi akuluwo anali pakhomo pa nyumba.
7 Nati kwa iwo, Muipse nyumbayi ndi kudzaza mabwalo ndi ophedwa, mukani. Ndipo anaturuka, nakantha m'mudzimo.
8 Ndipo kunali, alimkukantha iwo, nditatsala ine, ndinagwa nkhope yanga pansi, ndi kupfuula, ndi kuti, Kalanga ine. Ambuye Mulungu! kodi mudzaononga otsala onse a Israyeli pakutsanulira ukali wanu pa Yerusalemu?
9 Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israyeli ndi Yuda ndi yaikurukuru ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mudziwo wadzala ndi kukhotetsa mirandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.
10 Ndipo Inenso diso langa silidzalekerera, wosacita cifundo Ine, koma ndidzawabwezera njira yao pamtu pao.
11 Ndipo taonani, munthu wobvala bafutayo, wokhala ndi zolembera nazo m'cuuno mwace, anabweza mau, ndi kuti, Ndacita monga munandilamulira ine.