12 Malo opatulika athu ndiwo mpando wacifumu wa ulemerero, wokhazikika pamsanje ciyambire.
13 Inu Yehova, ciyembekezo ca Israyeli, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondicokera Ine adzalembedwa m'dothi, cifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.
14 Mundiciritse ine, Yehova, ndipo ndidzaciritsidwa; mundipulumutse ine, ndipo ndidzapulumutsidwa; pakuti cilemekezo canga ndinu.
15 Taonani, ati kwa ine, Mau a Yehova ali kuti? adze tsopano.
16 Koma ine, pokhala mbusa sindinafulumira kucokerako kuti ndikutsateni Inu; sindinakhumba tsiku la tsoka; Inu mudziwa, cimene cinaturuka pa milomo yanga cinali pamaso panu.
17 Musakhale wondiopsetsa ine; ndinu pothawira panga tsiku la coipa.
18 Iwo akhale ndi manyazi amene andisautsa ine, koma ine ndisakhale ndi manyazi; aopsedwe iwo, koma ndisaopsedwe ine; muwatengere iwo tsiku la coipa, muwaononge ndi cionongeko cowirikiza.