5 Atero Yehova: Wotembereredwa munthu amene akhulupirira munthu, natama mkono wanyama, nucoka kwa Yehova mtima wace.
6 Ndipo adzakhala ngati tsanya la m'cipululu, ndipo saona pamene cifika cabwino; koma adzakhala m'malo oumitsa m'cipululu, dziko lacikungu lopanda anthu.
7 Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene cikhulupiriro cace ndi Yehova.
8 Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuti madzi, wotambalitsa mizu yace pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lace likhala laliwisi; ndipo subvutika cakaca cirala, suleka kubala zipatso.
9 Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosaciritsika, ndani angathe kuudziwa?
10 Ine Yehova ndisanthula mtima, ndiyesa imso, kuti ndimpatse munthu yense monga mwa njira zace, monga zipatso za nchito zace.
11 Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikira, momwemo iye amene asonkhanitsa cuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ace cidzamsiya iye, ndipo pa citsirizo adzakhala wopusa.