17 Koma maso ako ndi mtima wako sizisamalira kanthu koma kusirira, ndi kukhetsa mwazi wosacimwa, ndi kusautsa, ndi zaciwawa, kuti uzicite.
18 Cifukwa cace Yehova atero za Yehoyakimu mwana wace wa Yosiya, mfumu ya Yuda: Sadzamlira iye, kuti, Kalanga ine mbale wanga! kapena, Kalanga ine mlongo wanga! Sadzamlira, kuti, Kalanga ine mbuye! kapena, Kalanga ine ulemerero wace!
19 Adzamuika monga kuika buru, adzamkoka nadzamponya kunja kwa zipata za Yerusalemu.
20 Kwera ku Lebano, nupfuule; kweza mau ako m'Basani; nupfuule m'Abarimu; pakuti mabwenzi ako onse atha,
21 Ndinanena ndi iwe m'phindu lako; koma unati, Sindidzamva. Awa ndi makhalidwe ako kuyambira ubwana wako, kuti sudamvera mau anga,
22 Mphepo idzadyetsa abusa ako onse, ndipo mabwenzi ako adzalowa m'ndende; ntheradi udzakhala ndi manyazi ndi kunyazitsidwa cifukwa ca coipa cako conse.
23 Iwe wokhala m'Lebano, womanga cisa cako m'mikungudza, udzacitidwa cisoni cacikuru nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!