6 Masiku ace Yuda adzapulumutsidwa, ndipo Israyeli adzakhala mokhazikika, dzina lace adzachedwa nalo, ndilo Yehova ndiye cilungamo cathu.
7 Cifukwa cace, taonani, masiku alinkudza, ati Yehova, amene sadzatinso, Pali Yehova, amene anakweza ana a Israyeli kuwaturutsa m'dziko la Aigupto;
8 koma, Pali Yehova, amene anakweza ndi kutsogolera mbeu za nyumba ya Israyeli kuwaturutsa m'dziko la kumpoto, ndi ku maiko onse kumene ndinawapitikitsirako, ndipo adzakhala m'dziko lao.
9 Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; cifukwa ca Yehova, ndi cifukwa ca mau ace opatulika.
10 Pakuti dziko ladzala ndi acigololo; pakuti cifukwa ca temberero dziko lilira, mabusa a kucipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siiri yabwino.
11 Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.
12 Cifukwa cace njira yao idzakhala kwa iwo yonga malo akuterereka m'mdima; adzacotsedwa, nadzagwa momwemo; pakuti ndidzawatengera zoipa, caka ca kulangidwa kwao, ati Yehova.