4 Ndipo mau a Yehova anadza kwa ine, kuti,
5 Cifukwa Yehova, Mulungu wa Israyeli, atero, Monga nkhuyu zabwino izi, momwemo ndidzasamalira am'nsinga a Yuda, amene ndawacotsera m'malo muno kunka ku dziko la Akasidi, kuwacitira bwino.
6 Pakuti ndidzaika maso anga pa iwo kuti ndiwacitire iwo bwino, ndipo ndidzawabwezanso ku dziko ili: ndipo ndidzamangitsa mudzi wao, osawapasula; ndi kuwabzyala, osawazula iwo.
7 Ndipo ndidzapatsa iwo mtima wakundidziwa, kuti ndine Yehova; nadzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wao; pakuti adzabwera kwa Ine ndi mtima wao.
8 Ndipo, monga nkhuyu zoipa, zosadyeka, poti nzoipa; ntheradi atero Yehova, Comweco ndidzapereka Zedekiya mfumu ya Yuda, ndi akulu ace, ndi otsala a m'Yerusalemu, amene atsala m'dziko ili, ndi amene akhala m'dziko la Aigupto.
9 Ndipo ndidzawapatsa akhale coopsetsa coipa ku maufumu a dziko lapansi; akhale citonzo ndi nkhani ndi coseketsa, ndi citemberero, monse m'mene ndidzawapitikitsiramo.
10 Ndipo ndidzatuma lupanga, ndi njala, ndi caola mwa iwo, mpaka athedwa m'dziko limene ndinapatsa iwo ndi makolo ao.