31 Pakuti mudzi uwu unali woutsa mkwiyo wanga ndi ukali wanga kuyambira tsiku lija anaumanga mpaka lero, kuti ndiucotse pamaso panga;
32 cifukwa ca zoipa zonse za ana a Israyeli ndi za ana a Yuda, zimene anandiputa nazo Ine, iwowo, mafumu ao, akulu ao, ansembe ao, aneneri ao, ndi anthu a Yuda, ndi okhala m'Yerusalemu.
33 Ndipo anandipatsa Ine mbuyo, si nkhope, ngakhale ndinawaphunzitsa, kuuka m'mamawa ndi kuwaphunzitsa, koma sanamvera kulangizidwa.
34 Koma anaika zonyansa zao m'nyumba yochedwa dzina langa, kuti aidetse.
35 Ndipo anamanga misanje ya Baala, iri m'cigwaca mwana wace wa Hinomu, kuti apitirize kumoto ana ao amuna ndi akazi cifukwa ca Moleki; cimene sindinauza, cimene sicinalowa m'mtima mwanga, kuti acite conyansa ici, cocimwitsa Yuda.
36 Cifukwa cace tsopano atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, za mudzi umene, munena inu, waperekedwa m'dzanja la mfumu ya Babulo ndi lupanga, ndi njala, ndi caola:
37 Taonani, ndidzawasokolotsa m'maiko monse, kumene ndinawapitikitsira ndi mkwiyo wanga, ndi m'kupsa mtima kwanga, ndi mu ukali waukuru, ndipo ndidzawabwezeranso kumalo kuno, ndipo ndidzawakhazikitsa mokhulupirika,