1 Caka cacisanu ndi cinai ca Zedekiya mfumu ya Yuda, mwezi wakhumi, anadza Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ndi nkhondo yace yonse, ndi kuumangira misasa.
2 Caka cakhumi ndi cimodzi ca Zedekiya, mwezi wacinai, tsiku lacisanu ndi cinai, mudzi unabooledwa.
3 Ndipo akuru onse a mfumu ya ku Babulo analowa, nakhala m'cipata capakati, Nerigalisarezara, Samgari Nebo, Sarisekimu, mkuru wa adindo, Nerigalisarezara mkuru wa alauli ndi akuru ena onse a mfumu ya ku Babulo.
4 Ndipo panali pamene Zedekiya mfumu ya Yuda ndi amuna onse a nkhondo anawaona, anathawa naturuka m'mudzi usiku, panjira pa munda wa mfumu, pa cipata ca pakati pa makoma awiri; ndipo iye anaturukira pa njira ya kucidikha.
5 Koma nkhondo ya Akasidi inawalondola, nimpeza Zedekiya m'zidikha za Yeriko; ndipo atamgwira, anamtengera kwa Nebukadirezara mfumu ya ku Babulo ku Ribila m'dziko la Hamati, ndipo iye ananena naye mlandu.
6 Pamenepo mfumu ya ku Babulo inapha ana a Zedekiya ku Ribila pamaso pace; mfumu ya ku Babulo niphanso aufulu onse a Yuda.
7 Ndipo anakolowola maso a Zedekiya, nammanga m'zigologolo, kunka naye ku Babulo.