1 MASOMPHENYA a Yesaya mwana wa Amozi, amene iye anaona, onena za Yuda ndi Yerusalemu, masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.
2 Imvani, miyamba inu, chera makutu, iwe dziko lapansi, cifukwa Yehova wanena, Ndakulitsa ndipo ndalera ana, ndipo iwo anandipandukira Ine.
3 Ng'ombe idziwa mwini wace, ndi buru adziwa pomtsekereza: koma Israyeli sadziwa, anthu anga sazindikira.
4 Mtundu wocimwa inu, anthu olemedwa ndi mphulupulu, mbeu yakucita zoipa, ana amene acita moononga, iwo amsiya Yehova, iwo amnyoza Woyera wa Israyeli, iwo adana naye nabwerera m'mbuyo.
5 Nanga bwanji mukali cimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.
6 Kucokera pansi pa phazi kufikira kumutu m'menemo mulibe cangwiro; koma mabala, ndi mikwingwirima, ndi zironda; sizinapole, ngakhale kumangidwa, ngakhale kupakidwa mafuta.