31 Madimena ali wothawathawa; okhala m'Gebimu asonkhanakutiathawe.
32 Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lace pa phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.
33 Taonani, Ambuye Yehova wa makamu adzasadza nthambi moopsya; ndipo zazitari msinkhu zidzadulidwa, ndipo zazitari zidzagwetsedwa.
34 Ndipo adzadula nkhalango za m'thengo ndi citsulo, ndipo Lebano adzagwa ndi wamphamvu.