1 Ndipo padzaturuka mphukira pa tsinde la Jese, ndi nthambi yoturuka m'mizu yace idzabala zipatso;
2 ndipo mzimu wa Yehova udzambalira iye mzimu wanzeru ndi wakuzindikira, mzimu wa uphungu ndi mphamvu, mzimu wakudziwa ndi wakuopa Yehova;
3 ndipo adzakondwera nako kumuopa Yehova, ndipo sadzaweruza monga apenya maso, sadzadzudzula mwamphekesera:
4 koma ndi cilungamo adzaweruza aumphawi, nadzadzudzulira ofatsa a m'dziko moongoka; ndipo adzamenya dziko lapansi ndi cibonga ca kukamwa kwace, nadzapha oipa ndi mpweya wa milomo yace.
5 Ndipo cilungamo cidzakhala mpango wa m'cuuno mwace, ndi cikhulupiriko cidzakhala mpango wa pa zimpsyo zace.
6 Mmbulu udzakhala pamodzi ndi mwana wa nkhosa, ndipo nyalugwe adzagona pansi ndi mwana wa mbuzi; ndipo mwana wa ng'ombe ndi mwana wa mkango ndi coweta conenepa pamodzi; ndipo mwana wamng'ono adzazitsogolera.