4 Ndi Hesiboni apfuula zolimba, ndi Eliale; mau ao amveka, ngakhale ku Yahazi; cifukwa cace amuna ankhondo a Moabu apfuula zolimba; moyo wace wanthunthumira m'kati mwace.
5 Mtima wanga upfuula cifukwa ca Moabu: akuru ace athawira ku Zoari, ku Eglatiselisiya; pakuti pa cikweza ca Luhiti akwera alikulira, pakuti m'njira ya Horanaimu akweza mpfuu wa cionongeko.
6 Pakuti pa madzi a Nimirimi padzakhala mabwinja; papeza udzu wafota, msipu watha.
7 Cifukwa cace zocuruka adazipeza, ndi zosungidwa zao adzazitenga kunka nazo ku mtsinje wa mabango.
8 Pakuti kulira kwamveka kuzungulira malire a Moabu; kukuwa kwace kwafikira ku Eglaimu, ndi kukuwa kwace kwafikira ku Beerelimu.
9 Pakuti madzi a Dimoni adzala mwazi; pakuti ndidzatengera zina pa! Dimoni, mkango pa iye amene anapulumuka ku Moabu, ndi pa otsala am'dziko.