1 Katundu wa Damasiko. Taonani, Damasiko wacotsedwa usakhalenso mudzi, ndimo udzangokhala muunda wopasudwa.
2 Midzi ya Aroeri yasiyidwa; idzakhala ya zoweta zogona pansi, opanda woziopsya.
3 Ku Efraimu sikudzakhalanso linga, ngakhale ufumu ku Damasiko, ngakhale otsala kwa Aramu; iwo adzakhala ngati ulemerero wa ana a Israyeli, ati Yehova wamakamu.
4 Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti ulemerero wa Yakobo udzakhala wopyapyala, ndi kunenepa kwa thupi lace kudzaonda.
5 Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosaceka, ndi dzanja lace lirikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'cigwa ca Refaimu.
6 Koma mudzasiyidwa m'menemo khunkha, monga ngati kugwedeza kwace kwa mtengo waazitona, zipatso ziwiri pena zitatu m'nsonga ya nthambi yosomphoka, zinai pena zisanu m'nthambi za kunthemba, za mtengo wobalitsa, ati Yehova, Mulungu wa Israyeli.