5 Inu a nyumba ya Yakobo, tiyeni, tiyende m'kuwala kwa Yehova.
6 Cifukwa inu mwasiya anthu anu a nyumba ya Yakobo, cifukwa kuti iwo adzazidwa ndi miyambo ya kum'mawa, ndipo ali olaula ngati Afilisti, naomba m'manja ndi ana a acilendo.
7 Dziko lao ladzala siliva ndi golidi, ngakhale cuma cao ncosawerengeka; dziko lao lidzalanso akavalo, ngakhale magareta ao ngosawerengeka.
8 Dziko lao ladzalanso mafano; iwo apembedza nchito ya manja ao ao, imene zala zao zao zinaipanga.
9 Munthu wacabe agwada pansi, ndi munthu wamkuru adzicepetsa, koma musawakhululukire.
10 Lowa m'phanga, bisala m'pfumbi, kucokera pa kuopsya kwa Yehova, ndi pa ulemerero wacifumu wace.
11 Maso a munthu akuyang'anira kumwamba adzatsitsidwa, ndi kudzikweza kwa anthu kudzaweramitsidwa pansi; ndipo Yehova yekha adzakwezedwa tsiku limenelo.