3 Ndipo Yehova anati, Monga mtumiki wanga Yesaya wayenda marisece ndi wopanda nsapato zaka zitatu, akhale cizindikilo ndi codabwitsa kwa Aigupto ndi kwa Etiopia;
4 momwemo mfumu ya Asuri idzatsogolera kwina am'nsinga a Aigupto, ndi opitikitsidwa a Etiopia, ana ndi okalamba, amarisece ndi opanda nsapato, ndi matako osabvala, kuti acititse manyazi Aigupto.
5 Ndipo iwo adzakhala ndi mantha ndi manyazi, cifukwa ca Kusi, amene anawatama, ndi Aigupto, amene anawanyadira.
6 Ndipo wokhala m'mphepete mwa nyanja muno adzati tsiku limenelo, Taonani, kuyembekeza kwathu kuli kotero, kumene ife tinathawira atithangate kupulumutsidwa kwa mfumu ya Asuri, ndipo ife tidzapulumuka bwanji?