13 Cifukwa cace padzakhala cotero pakati pa dziko mwa anthu, ngati kugwedeza kwa mtengo waazitona, ngati khunkha la mphesa, pakutha masika ace.
14 Amenewa adzakweza mau ao, nadzapfuula; cifukwa ca cifumu ca Yehova, iwo adzapfuula zolimba panyanja.
15 Cifukwa cace lemekezani inu Yehova kum'mawa, ngakhale dzina la Yehova, Mulungu wa Israyeli, m'zisumbu za m'nyanja.
16 Kucokera ku malekezero a dziko ife tamva nyimbo zolemekeza wolungama. Koma ine ndinati, Ndaonda ine, ndaonda ine, tsoka kwa ine! amalonda onyenga amangonyenga; inde ogulitsa onyenga apambana kunyenga.
17 Mantha ndi dzenje ndi msampha ziri pa iwe, wokhala m'dziko.
18 Ndipo padzali, kuti iye amene athawa mbiri yoopsya, adzagwa m'dzenje; ndi iye amene aturuka m'kati mwa dzenje, adzakodwa mumsampha, pakuti mazenera a kuthambo atsegudwa, ndi maziko a dziko agwedezeka.
19 Dziko lapansi lasweka ndithu, dziko lapansi lasungunukadi, dziko lapansi liri kugwedezeka kopambana.