11 Iai, koma ndi anthu a milomo yacilendo, ndi a lilume lina, Iye adzalankhula kwa anthu awa;
12 amene ananena nao, Uku ndi kupuma, mupumitsa wolema, ndi apa ndi potsitsimutsa, koma iwo anakana kumva.
13 Cifukwa cace mau a Yehova adzakhala kwa iwo langizo ndi langizo, langizo ndi langizo; lamulo ndi lamulo, lamulo ndi lamulo; kuno pang'ono, uko pang'ono; kuti ayende ndi kugwa cambuyo, ndi kutyoka, ndi kukodwa mumsampha, ndi kugwidwa.
14 Cifukwa cace imvani mau a Yehova, inu amuna amnyozo, olamulira anthu awa a m'Yerusalemu.
15 Cifukwa inu munati, Ife tapangana pangano ndi imfa, tabvomerezana ndi kunsi kwa manda; pakuti mliri wosefukira sudzatifikira ife; pakuti tayesa mabodza pothawirapo pathu, ndi kubisala m'zonyenga;
16 cifukwa cace Ambuye Yehova atero, Taonani, ndiika m'Ziyoni mwala wa maziko, mwala woyesedwa mwala wa pangondya, wa mtengo wace wokhazikika ndithu; wokhulupirira sadzafulumira.
17 Ndipo ndidzayesa ciweruziro cingwe coongolera, ndi cilungamo cingwe colungamitsira ciriri; ndipo matalala adzacotsa pothawirapo mabodza, ndi madzi adzasefukira mobisalamo.