1 Idzani pafupi, amitundu inu, kuti mumve; mverani anthu inu, dziko limve, ndi za mommo; dziko ndi zinthu zonse zoturukamo.
2 Pakuti Yehova akwiyira amitundu onse, nacitira ukali khamu lao lonse; Iye wawaononga psiti, wawapereka kukaphedwa,
3 Ophedwa aonso adzatayidwa kunja, ndipo kununkha kwa mitembo yao kudzamveka, ndipo mapiri adzasungunuka ndi mwazi wao.
4 Ndipo makamu onse a kumwamba adzasungunuka, ndi miyamba idzapindika pamodzi ngati mpukutu; makamu ao onse adzafota monga tsamba limafota pampesa ndi kugwa, ndi monga tsamba lifota pamkuyu.
5 Pakuti lupanga langa lakhuta kumwamba; taonani, lidzatsikira pa Edomu, ndi pa anthu amene ndawatemberera, kuti aweruzidwe.
6 Lupanga la Yehova lakhuta ndi mwazi, lanona ndi mafuta ndi mwazi wa ana a nkhosa, ndi mbuzi, ndi mafuta a imso ya nkhosa zamphongo; pakuti Yehova ali ndi nsembe m'Bozira, ndi ophedwa ambiri m'dziko la Edomu.
7 Ndipo njati zidzatsika ndi iwo, ndi ng'ombe zofula ndi zamphongo; ndi dziko lao lidzakhuta ndi mwazi, ndi pfumbi lao lidzanona ndi mafuta.