14 Ndipo zirombo za m'cipululu zidzakomana ndi mimbulu, tonde adzaitana mnzace; inde mancici adzatera kumeneko, nadzapeza popumira.
15 Kumeneko njoka yotumpha idzapanga cisanja cace, niikira, niumatira, niswa mumthunzi mwace; inde kumeneko miimba idzasonkhana wonse ndi unzace.
16 Funani inu m'buku la Yehova, nimuwerenge; palibe umodzi wa iye udzasowa, palibe umodzi udzasowa unzace; pakuti pakamwa pa Yehova panena, ndipo mzimu wace wasonkhanitsa iwo.
17 Ndipo Iye wacita maere, cifukwa ca zirombozi, ndipo dzanja lace lazigawira dzikolo ndi cingwe, zidzakhala nalo nthawi zonse ku mibadwo mibadwo, zidzakhala m'menemo.