3 Mau a wopfuula m'cipululu, Konzani njira ya Yehova, lungamitsani m'dziko loti se khwalala la Mulungu wathu.
4 Cigwa ciri conse cidzadzazidwa, ndipo phiri liri lonse ndi citunda ciri conse zidzacepetsedwa, ndipo zokhota zidzaongoledwa, ndipo zamakolokoto zidzasalala;
5 ndipo ulemerero wa Yehova udzabvumbulutsidwa, ndipo anthu onse adzauona pamodzi, pakuti pakamwa pa Yehova panena comweco,
6 Mau a wina ati, Pfuula. Ndipo ndinati, Kodi ndipfuule ciani? Anthu onse ndi udzu, ndi kukoma kwao konse kunga duwa la m'thengo;
7 udzu unyala, duwa lifota; cifukwa mpweya wa Yehova waombapo; zoonadi anthu ndi udzu.
8 Udzu unyala, duwa lifota, koma mau a Mulungu wathu adzakhala nthawi zacikhalire.
9 Iwe amene utengera mau abwino ku Ziyoni, kwera iwe pamwamba pa phiri lalitari; iwe amene utengera mau abwino ku Yerusalemu, kweza mau ako ndi mphamvu, kwezetsa usaope, nena ku midzi ya Yuda, Taonani, Mulungu wanu!