7 Cotero mmisiri wa mitengo analimbikitsa wosula golidi, ndi iye amene asalaza ndi nyundo anamlimbikitsa iye amene amenya posulira, nanena za kulumikiza ndi nthobvu, Kuti kwabwino; ndipo iye akhomera fanolo misomali kuti lisasunthike.
8 Koma iwe, Israyeli, mtumiki wanga, Yakobo, amene ndinakusankha, mbeu ya Abrahamu bwenzi langa;
9 iwe amene ndinakuwira iwe zolimba kucokera ku malekezero a dziko lapansi, ndi kukuitana iwe kucokera m'ngondya zace, ndipo ndinati kwa iwe, Ndiwe mtumiki wanga ndakusankha, sindinakutaya kunja;
10 usaope, pakuti Ine ndiri pamodzi ndi iwe; usaopsyedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakucirikiza ndi dzanja langa lamanja la cilungamo.
11 Taona, onse amene akukwiyira iwe adzakhala ndi manyazi, nasokonezedwa; iwo amene akangana ndi iwe adzakhala ngati cabe, nadzaonongeka.
12 Iwe udzawafuna osawapeza, ngakhale iwo amene akangana ndi iwe; ocita nkhondo ndi iwe, adzakhala ngati cabe, ndi monga kanthu kopanda pace.
13 Pakuti Ine Yehova Mulungu wako ndidzagwira dzanja lako lamanja, ndi kunena kwa iwe, Usaope ndidzakuthandiza iwe.