9 Amitundu onse asonkhane pamodzi, ndi anthu aunjikane; ndani mwa iwo anganene ici ndi kuonetsa ife zinthu zakale? atenge mboni zao, kuti abvomerezeke ndi olungama; pena amve, nanene zoonadi.
10 Inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; kuti mundidziwe, ndi kundikhulupirira Ine, ndi kuzindikira, kuti Ine ndine; ndisanakhale Ine, panalibe Mulungu wolengedwa, ngakhale pambuyo panga sipadzakhala wina.
11 Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.
12 Ine ndalalikira, ndipo ndikupulumutsa ndi kumvetsa, ndipo panalibe Mulungu wacilendo pakati pa inu; cifukwa cace inu ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndipo Ine ndine Mulungu.
13 Inde ciyambire nthawi Ine ndine, ndipo palibe wina wopulumutsa m'dzanja langa; ndidzagwira nchito, ndipo ndani adzaletsa?
14 Atero Yehova, Mombolo wanu, Woyera wa Israyeli: Cifukwa ca inu ndatumiza ku Babulo, ndipo ndidzatsitsira iwo onse monga othawa, ngakhale Akasidi m'ngalawa za kukondwa kwao.
15 Ine ndine Yehova Woyera wanu, Mlengi wa Israyeli, Mfumu yanu,