4 ndipo iwo adzaphuka pakati pa maudzu, ngati msondodzi m'mphepete mwa madzi.
5 Wina adzati, Ine ndiri wa Yehova; ndi wina adzadzicha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lace, Ndine wa Yehova, ndi kudzicha yekha ndi mfunda wa lsrayeli.
6 Atero Yehova, Mfumu ya Israyeli ndi Mombolo wace, Yehova wa makamu, Ine ndiri woyamba ndi womariza, ndi popanda Ine palibenso Mulungu.
7 Ndipo ndani adzaitana monga Ine, ndi kulalikira ici ndi kundilongosolera ici, cikhazikitsire Ine anthu akale? milunguyo iwadziwitse zomwe zirinkudza, ndi za m'tsogolo.
8 Musaope inu, musakhale ndi mantha; kodi ndinanena kwa iwe zakale, ndi kuzionetsa zimenezo, ndipo inu ndinu mboni zanga. Kodi popanda Ine aliponso Mulungu? Iai, palibe thanthwe; sindidziwa liri lonse.
9 Omwe apanga fano losema onsewo asokonezeka; ndipo zokondweretsa zao sadzapindula nazo kanthu; ndipo mboni zao siziona, kapena kudziwa; kuti akhale ndi manyazi.
10 Ndani wapanga mulungu, kapena kusungunula fano losema losapindula kanthu?