1 Atero Yehova kwa wodzozedwa wace kwa Koresi, amene dzanja lace lamanja ndaligwiritsa, kuti agonjetse mitundu ya anthu pamaso pace, ndipo ndidzamasula m'cuuno mwa mafumu; atsegule zitseko pamaso pace, ndi zipata sizidzatsekedwa:
2 Ndidzakutsogolera ndi kusalaza pokakala; ndidzatyolatyola zitseko zamkuwa, ndi kudula pakati akapici acitsulo;
3 ndipo ndidzakupatsa iwe cuma ca mumdima, ndi zolemera zobisika za m'malo am'tseri, kuti iwe udziwe kuti Ine ndine Yehova, amene ndikuitana iwe dzina lako, ndine Mulungu wa Israyeli.
4 Ndakuitana iwe dzina lako, cifukwa ca Yakobo mtumiki wanga ndi Israyeli wosankhidwa wanga; ndakuonjezera dzina, ngakhale iwe sunandidziwa Ine.
5 Ine ndiri Yehova, ndipo palibe winanso; popanda Ine palibe Mulungu; ndidzakumanga m'cuuno, ngakhale sunandidziwa;
6 kuti anthu akadziwe kucokera ku maturukiro a dzuwa ndi kumadzulo, kuti palibe wina popanda Ine; Ine ndine Yehova, palibe winanso.