10 Tsoka kwa iye amene ati kwa atate wace, Kodi iwe ubalanji? pena kwa mkazi, Ulikusauka ninji iwe?
11 Atero Yehova Woyera wa Israyeli ndi Mlengi wace, Ndifunse Ine za zinthu zimene zirinkudza; za ana anga amuna, ndi za nchito ya manja anga, ndilamulireni Ine.
12 Ine ndalenga dziko lapansi, ndalengamo munthu; Ine, ngakhale manja anga, ndafunyulula kumwamba, ndi zonse za m'menemo, ndinazilamulira ndine.
13 Ine ndautsa Koresi m'cilungamo, ndipo ndidzalungamitsa njira zace zonse; iye adzamanga mudzi wanga, nadzaleka andende anga anke mwa ufulu, wosati ndi mtengo pena mphotho, ati Yehova wa makamu.
14 Atero Yehova, Nchito ya Aigupto, ndi malonda a Kusi, ndi a Sabea, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.
15 Ndithu Inu ndinu Mulungu, amene mudzibisa nokha, Mulungu wa Israyeli, Mpulumutsi.
16 Iwo adzakhala ndi manyazi, inde, adzathedwa nzeru onsewo; adzalowa m'masokonezo pamodzi, amene apanga mafano.