16 Idzani inu cifupi ndi Ine, imvani ici; kuyambira pa ciyambi sindinanene m'tseri; ciyambire zimenezi, Ine ndiripo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wace.
17 Atero Yehova, Mombolo wako, Woyera wa Israyeli, Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m'njira yoyenera iwe kupitamo.
18 Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi cilungamo cako monga mafunde a nyanja;
19 mbeu yakonso ikadakhala monga mcenga ndi obadwa a m'cuuno mwako momwemo; dzina lace silikadacotsedwa, pena kuonongeka pamaso panga.
20 Turukani inu m'Babulo, athaweni Akasidi; ndi mau akuyimba nenani inu, bukitsani ici, lalikirani ici, ngakhale ku malekezero a dziko; nenani, Yehova waombola mtumiki wace Yakobo.
21 Ndipo iwo sanamva ludzu, pamene Iye anawatsogolera m'mapululu; anawaturutsira madzi kuturuka m'matanthwe; anadulanso thanthwe, madzi nabulika.
22 1 Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.