4 Popeza ndinadziwa, kuti uli wokanika, ndi khosi lako liri mtsempha wacitsulo, ndi mphumi yako mkuwa;
5 cifukwa cace ndinakudziwitsa ici kuyambira kale; cisanaoneke ndinakusonyeza ico, kuti iwe unganene, Fano langa lacita izo, ndi cifanizito canga cosema, ndi cifaniziro canga coyenga zinazilamulira.
6 Iwe wacimva taona zonsezi; ndipo inu kodi inu simudzacinena? Ndakusonyeza iwe zinthu zatsopano kucokera nthawi yino, ngakhale zinthu zobisika, zimene iwe sunazidziwe.
7 Zalengedwa tsopano, zosati kuyambira kale; ndipo lisanafike tsiku laleroli iwe sunazimve; unganene, Taonani, ndinazidziwa.
8 Inde, iwe sunamva; inde, sunadziwe; inde, kuyambira kale khutu lako silinatsegudwe; pakuti ndinadziwa kuti iwe wacita mwaciwembu ndithu, ndipo unayesedwa wolakwa cibadwire.
9 Cifukwa ca dzina langa ndidzacedwetsa mkwiyo wanga, ndi cifukwa ca kutamanda kwanga ndidzakulekerera, kuti ndisakucotse.
10 Taona ndakuyenga, koma si monga siliva, ndakuyesa iwe m'ng'anjo ya masautso.