1 Mverani Ine, zisumbu inu, mumvere anthu inu akutari; Yehova anandiitana Ine ndisanabadwe; m'mimba mwa amai Iye anachula dzina langa;
2 nacititsa pakamwa panga ngati lupanga lakuthwa, mu mthunzi wa dzanja lace wandibisa Ine; wandipanga Ine mubvi wotuulidwa; m'phodo mwace Iye wandisungitsa Ine, nati kwa Ine,
3 Iwe ndiwe mtumiki wanga, Israyeli, amene ndidzalemekezedwa nawe.
4 Koma ndinati, Ndagwira nchito mwacabe, ndatha mphamvu zanga pacabe, ndi mopanda pace; koma ndithu ciweruziro canga ciri ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.