3 Iwe ndiwe mtumiki wanga, Israyeli, amene ndidzalemekezedwa nawe.
4 Koma ndinati, Ndagwira nchito mwacabe, ndatha mphamvu zanga pacabe, ndi mopanda pace; koma ndithu ciweruziro canga ciri ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.
5 Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wace, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israyeli asonkhanidwe kwa Iye; cifukwa Ine ndiri wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;
6 inde, ati, Ciri cinthu copepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israyeli; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale cipulumutso canga mpaka ku malekezero a dziko lapansi.
7 Atero Yehova, Mombolo wa Israyeli, ndi Woyera wace, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyansidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira cifukwa ca Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israyeli, amene anakusankha Iwe.
8 Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la cipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;
9 ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m'njira, ndi m'zitunda zonse zoti se mudzakhala busa lao.