Yesaya 49:4-10 BL92

4 Koma ndinati, Ndagwira nchito mwacabe, ndatha mphamvu zanga pacabe, ndi mopanda pace; koma ndithu ciweruziro canga ciri ndi Yehova, ndi kubwezera kwanga kuli ndi Mulungu wanga.

5 Ndipo tsopano, ati Yehova, amene anandiumba Ine ndisanabadwe ndikhale mtumiki wace, kubwezanso Yakobo kwa Iye, ndi kuti Israyeli asonkhanidwe kwa Iye; cifukwa Ine ndiri wolemekezeka pamaso pa Yehova, ndipo Mulungu wanga wakhala mphamvu zanga;

6 inde, ati, Ciri cinthu copepuka ndithu kuti Iwe ukhale mtumiki wanga wakuutsa mafuko a Yakobo, ndi kubwezera osungika a Israyeli; ndidzakupatsanso ukhale kuunika kwa amitundu, kuti ukhale cipulumutso canga mpaka ku malekezero a dziko lapansi.

7 Atero Yehova, Mombolo wa Israyeli, ndi Woyera wace, kwa Iye amene anthu amnyoza, kwa Iye amene mtundu wathu unyansidwa naye, kwa mtumiki wa olamulira: Mafumu adzaona, nadzauka; akalonga nadzalambira cifukwa ca Yehova, amene ali wokhulupirika, ngakhale Woyera wa Israyeli, amene anakusankha Iwe.

8 Atero Yehova, Nthawi yondikomera ndakuyankha Iwe, ndi tsiku la cipulumutso ndakuthandiza; ndipo ndidzakusunga ndi kupatsa Iwe ukhale pangano la anthu, kuti ukhazikitse dziko, nuwalowetse m'zolowa zopasuka m'malo abwinja;

9 ndi kunena kwa iwo amene ali omangidwa, Mukani, kwa iwo amene ali mumdima, Dzionetseni nokha. Iwo adzadya m'njira, ndi m'zitunda zonse zoti se mudzakhala busa lao.

10 Iwo sadzakhala ndi njala, pena ludzu; ngakhale thukuta, pena dzuwa silidzawatentha; pakuti Iye amene wawacitira cifundo, adzawatsogolera, ngakhale pa akasupe a madzi adzawatsogolera.