2 Dzisanse pfumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni.
3 Pakuti atero Yehova, Inu munagulitsidwa cabe, ndipo mudzaomboledwa opanda ndalama.
4 Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Aigupto poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asuri anawatsendereza popanda cifukwa.
5 Cifukwa cace kodi ndicitenji pano? ati Yehova; popeza anthu anga acotsedwa popanda kanthu? akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa licitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.
6 Cifukwa cace anthu anga adzadziwa dzina langa; cifukwa cacersiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.
7 Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa cipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.
8 Mau a alonda ako! akweza mau, ayimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni.