1 Yimba, iwe wouma, amene sunabala; yimba zolimba ndi kupfuula zolimba, iwe amene sunabala mwana; pakuti ana a mfedwa acuruka koposa ana a mkazi wokwatibwa ndi mwamuna, ati Yehova.
2 Kuza malo a hema wako, afunyulule zinsaru za mokhalamo iwe; usaleke, tanimphitsa zingwe zako, limbitsa zikhomo zako.
3 Pakuti iwe udzafalikira ponse pa dzanja lamanja ndi lamanzere, ndipo mbeu yako idzalandira amitundu colowa cao, ndi kukhalitsa anthu m'mabwinja.
4 Usaope, pakuti sudzakhala ndi manyazi; usasokonezedwe, pakuti sudzacitidwa manyazi; pakuti udzaiwala manyazi a ubwana wako, ndi citonzo ca umasiye wako sudzacikumbukiranso.
5 Pakuti Mlengi wako ndiye mwamuna wako; Yehova wa makamu ndiye dzina lace; ndi Woyera wa Israyeli ndiye Mombolo wako; Iye adzachedwa Mulungu wa dziko lonse lapansi.
6 Pakuti Yehova wakuitana iwe monga mkazi wakusiyidwa ndi wosauka m'mzimu, ngakhale mkazi wa ubwana wocotsedwa, ati Mulungu wako.
7 Kamphindi kakang'ono ndakusiya iwe, koma ndi cifundo cambiri ndidzakusonkhanitsa.