1 Ndani uyu alinkudza kucokera ku Edomu, ndi zobvala zonika zocokera ku Bozira? uyu wolemekezeka m'cobvala cace, nayenda mu ukuru wa mphamvu zace? Ndine amene ndilankhula m'colungama, wa mphamvu yakupulumutsa,
2 Cophimba cako cifiiriranji, ndi zobvala zako zifanana bwanji ndi woponda mopondera mphesa?
3 Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga: ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zobvala zanga; ndipo ndadetsa copfunda canga conse.
4 Pakuti tsiku lakubwezera liri mumtima mwanga, ndi caka ca kuombola anthu anga cafika.
5 Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wocirikiza; cifukwa cace mkono wanga wanga unanditengera cipulumutso, ndi ukali wanga unandicirikiza Ine.