2 Cophimba cako cifiiriranji, ndi zobvala zako zifanana bwanji ndi woponda mopondera mphesa?
3 Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga: ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zobvala zanga; ndipo ndadetsa copfunda canga conse.
4 Pakuti tsiku lakubwezera liri mumtima mwanga, ndi caka ca kuombola anthu anga cafika.
5 Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wocirikiza; cifukwa cace mkono wanga wanga unanditengera cipulumutso, ndi ukali wanga unandicirikiza Ine.
6 Ndipo ndinapondereza anthu m'kukwiya kwanga, ndi kuwatswanya mu ukali wanga, ndi kutsanulira mwazi wa moyo wao.
7 Ndidzachula za cifundo cace ca Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wace waukuru kwa banja la Israyeli, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa cifundo cace, ndi monga mwa nchito zocuruka za cikondi cace.
8 Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangacite monyenga; comweco Iye anali Mpulumutsi wao.