10 Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati,
11 Udzipemphere wekha cizindikilo ca kwa Yehova Mulungu wako; pempha cam'mwakuya, kapena cam'mwamba.
12 Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova.
13 Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga?
14 Cifukwa cace Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu cizindikilo; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamucha dzina lace Imanueli.
15 Iye adzadya mafuta ndi uci, pamene adziwa kukana coipa ndi kusankha cabwino.
16 Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana coipa ndi kusankha cabwino, dziko limene mafumu ace awiri udana nao lidzasyidwa.