11 Cifukwa cace Yehova adzamkwezera Rezini olimbana naye, nautsa adani ace;
12 Aramu patsogolo ndi Afilisti pambuyo; ndipo iwo adzadya Israyeli ndi kukamwa koyasama. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.
13 Koma anthu sanatembenukire kwa Iye amene anawamenya, ngakhale kufuna Yehova wa makamu.
14 Cifukwa cace Yehova adzadula mutu wa Israyeli ndi mcira wace; nthambi ya kanjedza ndi mlulu, tsiku limodzi.
15 Nkhalamba ndi wolemekezeka ndiye mutu, ndi mneneri wophunzitsa zonama ndiye mcira.
16 Pakuti iwo amene atsogolera anthuwa, ndiwo awasokeretsa; ndipo iwo amene atsogoleredwa nao aonongeka.
17 Cifukwa cace Ambuye sadzakondwera ndi anyamata ao, ngakhale kuwacitira cifundo amasiye ao ana ndi akazi; popeza yense ali wodetsa ndi wocimwa, m'kamwa monse mulankhula zopusa. Mwa izi zonse mkwiyo wace sunacoke, koma dzanja lace liri citambasulire.